Publicidade

Salmos 126

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

1 Yehova atabwezera akapolo ku Ziyoni,

tinali ngati amene akulota.

2 Pakamwa pathu panadzaza ndi kuseka;

malilime athu ndi nyimbo zachimwemwe.

Pamenepo kunanenedwa pakati pa anthu kuti,

"Yehova wawachitira zinthu zazikulu."

3 Yehova watichitira zinthu zazikulu,

ndipo tadzazidwa ndi chimwemwe.

4 Tibwezereni madalitso athu, Inu Yehova,

monga mitsinje ya ku Negevi.

5 Iwo amene amafesa akulira,

adzakolola akuyimba nyimbo zachimwemwe.

6 Iye amene amayendayenda nalira,

atanyamula mbewu yokafesa,

adzabwerera akuyimba nyimbo zachimwemwe,

atanyamula mitolo yake.

Veja também

Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-07-04_15-35-42-