Pular para o conteúdo
Publicidade

MASALIMO 66

1 Fuwulani kwa Mulungu ndi chimwemwe, dziko lonse lapansi!

2 Imbani ulemerero wa dzina lake;

kumutamanda kwake kukhale kwaulemerero.

3 Nenani kwa Mulungu, "Ntchito zanu ndi zoopsa ndithu!

Mphamvu yanu ndi yayikulu kwambiri

kotero kuti adani anu amawerama pamaso panu.

4 Dziko lonse lapansi limaweramira inu;

limayimba matamando kwa Inu;

limayimba matamando pa dzina lanu."

Sela.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.

Veja também