4 Sitidzabisira ana awo,
tidzafotokozera mʼbado wotsatira
ntchito zotamandika za Yehova,
mphamvu zake, ndi zozizwitsa zimene Iye wachita.
5 Iye anapereka mawu wodzichitira umboni kwa Yakobo
ndi kukhazikitsa lamulo mu Israeli,
zimene analamulira makolo athu
kuphunzitsa ana awo,
6 kotero kuti mʼbado wotsatira uthe kuzidziwa,
ngakhale ana amene sanabadwe,
ndi kuti iwo akafotokozere ana awonso.
7 Choncho iwo adzakhulupirira Mulungu
ndipo sadzayiwala ntchito zake
koma adzasunga malamulo ake.