Pular para o conteúdo
Publicidade

MASALIMO 91

1 Iye amene amakhala mu mthunzi wa Wammwambamwamba

adzapuma mu mthunzi wa Wamphamvuzonse.

2 Ndidzanena za Yehova, "Iye ndiye pothawira panga ndi linga langa,

Mulungu wanga amene ndimadalira."

3 Ndithu, Iye adzakupulumutsa ku msampha wa mlenje

ndi ku mliri woopsa;

4 Adzakuphimba ndi nthenga zake,

ndipo udzapeza malo othawira mʼmapikomo;

kukhulupirika kwake kudzakhala chishango chako ndi lihawo.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.

Veja também