Salimo. Nyimbo ya pa tsiku la Sabata.
1 Nʼkwabwino kutamanda Yehova
ndi kuyimbira nyimbo dzina lanu, Inu Wammwambamwamba,
2 Kulengeza chikondi chanu mmawa,
ndi kukhulupirika kwanu nthawi ya usiku,
3 kuyimbira nyimbo choyimbira cha zingwe khumi
ndi mayimbidwe abwino a zeze.